Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 9:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 ndipo anawuza Moseyo kuti, “Ife tadetsedwa chifukwa cha mtembo wa munthu. Nʼchifukwa chiyani taletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena pa nthawi yake?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, pakati pa ana a Israele?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, pakati pa ana a Israele?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Anthuwo adauza Mose kuti, “Ife ndife oipitsidwa chifukwa tidakhudza mtembo wa munthu. Chifukwa chiyani tikuletsedwa kubwera ndi zopereka zathu kwa Chauta pa nthaŵi yake pakati pa anzathu Aisraele?”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:7
7 Mawu Ofanana  

Inu mukawawuze kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Yehova, popeza pamene ankakantha nyumba za Aigupto anasiya nyumba zathu.’ ” Kenaka anthu anawerama napembedza.


“Aisraeli azichita Paska pa nthawi yake yoyikika.


Koma ena a iwo sanathe kuchita nawo Paska pa tsiku limenelo chifukwa anali odetsedwa chifukwa chokhudza mtembo. Choncho anabwera kwa Mose ndi Aaroni tsiku lomwelo,


Mose anawayankha kuti, “Dikirani mpaka nditamva zimene Yehova walamula zokhudza Inu.”


Mumuphere Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, chiweto chochokera pa nkhosa zanu kapena ngʼombe zanu kumalo kumene Yehova adzasankha kuti akhazikeko dzina lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa