Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, chifukwa cha mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azichitira Yehova Paska.
Numeri 9:11 - Buku Lopatulika Mwezi wachiwiri, tsiku lake lakhumi ndi chinai, madzulo, auchite; audye ndi mkate wopanda chotupitsa ndi msuzi wowawa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwezi wachiwiri, tsiku lake lakhumi ndi chinai, madzulo, auchite; audye ndi mkate wopanda chotupitsa ndi msuzi wowawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Achite pa mwezi wachiŵiri, pa tsiku la 14, madzulo ake. Adye nyama ya Paskayo pamodzi ndi buledi wosafufumitsa ndi ndiwo zoŵaŵa zamasamba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Azichita chikondwererochi madzulo a pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Azidya mwana wankhosa wamwamuna pamodzi ndi buledi wopanda yisiti ndi ndiwo zowawa zamasamba. |
Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, chifukwa cha mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azichitira Yehova Paska.
Tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, muziuchita, pa nyengo yake yoikidwa; muuchite monga mwa malemba ake onse, ndi maweruzo ake onse.
Musamadyera nayo mkate wa chotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda chotupitsa, ndiwo mkate wa chizunziko popeza munatuluka m'dziko la Ejipito mofulumira; kuti mukumbukire tsiku lotuluka inu m'dziko la Ejipito masiku onse a moyo wanu.