Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kuchita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa mwezi wachiwiri, msonkhano waukulu ndithu.
Numeri 9:10 - Buku Lopatulika Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, chifukwa cha mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azichitira Yehova Paska. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, chifukwa cha mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azichitira Yehova Paska. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uza Aisraele kuti, munthu wina aliyense mwa inu, kapena mwa zidzukulu zanu, akadziipitsa pokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala paulendo, achitebe Paska ya Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene wina mwa inu kapena zidzukulu zanu adetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala pa ulendo, akhoza kuchita nawo Paska ya Yehova. |
Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kuchita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa mwezi wachiwiri, msonkhano waukulu ndithu.
Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efuremu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretse, koma anadya Paska mosati monga munalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense
Pakuti mfumu idapangana ndi akulu ake, ndi msonkhano wonse wa mu Yerusalemu, kuti achite Paska mwezi wachiwiri.
Mwezi wachiwiri, tsiku lake lakhumi ndi chinai, madzulo, auchite; audye ndi mkate wopanda chotupitsa ndi msuzi wowawa.
usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.
Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.