Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 8:21 - Buku Lopatulika

Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zovala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawachitira chotetezera kuwayeretsa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zovala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawachitira chotetezera kuwayeretsa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Alevi adadziyeretsa ku zoipa, ndipo adachapa zovala zao. Aroni adaŵapereka kuti akhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta, naŵachitira mwambo wopepesera machimo ao, kuti aŵayeretse.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Alevi anadziyeretsa ndi kuchapa zovala zawo. Kenaka Aaroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe yopepesera machimo yowayeretsa.

Onani mutuwo



Numeri 8:21
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.


Ndipo wansembe amene amyeretsayo, amuike munthu uja wakuti ayeretsedwe, ndi zinthu zija, pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako;


iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri.


Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lachitatu, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri amyeretse; ndipo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala woyera madzulo.


Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga.


Ndipo atatero alowe Alevi kuchita ntchito ya chihema chokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula.


Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele anachitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a Israele anawachitira.


Ndipo atatero, Alevi analowa kuchita ntchito yao m'chihema chokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake aamuna; monga Yehova analamula Mose kunena za Alevi, momwemo anawachitira.


Ndipo utere nao kuwayeretsa: uwawaze madzi akuchotsa zoipa, ndipo apititse lumo pa thupi lao lonse, natsuke zovala zao, nadziyeretse.