ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
Numeri 8:15 - Buku Lopatulika Ndipo atatero alowe Alevi kuchita ntchito ya chihema chokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atatero alowe Alevi kuchita ntchito ya chihema chokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Aleviwo adzaloŵa kuti atumikire m'chihema chamsonkhano, utaŵayeretsa ndi kuŵapereka ngati chopereka choweyula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Utatha kuyeretsa ndi kupereka Aleviwo monga nsembe yoweyula, apite kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano. |
ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga.
ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova.
Ndipo uimike Alevi pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula kwa Yehova.
Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele.