Numeri 7:30 - Buku Lopatulika Tsiku lachinai Elizuri, mwana wa Sedeuri, kalonga wa ana a Rubeni: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku lachinai Elizuri, mwana wa Sedeuri, kalonga wa ana a Rubeni: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lachinai linali la Elizuri mwana wa Sedeuri, mtsogoleri wa Arubeni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lachinayi linali la Elizuri mwana wa Sedeuri, mtsogoleri wa fuko la Rubeni, anabweretsa chopereka chake. |
Mbendera ya chigono cha Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri.
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyabu mwana wa Heloni.
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika, zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;