Ichi ndi chilamulo cha Mnaziri wakuwinda, ndi cha chopereka chake cha Yehova chifukwa cha kusala kwake, pamodzi nacho chimene dzanja lake likachipeza; azichita monga mwa chowinda chake anachiwinda, mwa chilamulo cha kusala.
Numeri 6:4 - Buku Lopatulika Masiku onse a kusala kwake asadye kanthu kopangika ndi mphesa, kuyambira nthanga zake kufikira khungu lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku onse a kusala kwake asadye kanthu kopangika ndi mphesa, kuyambira nthanga zake kufikira khungu lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Masiku onse pamene munthuyo ali wodzipereka kwa Chauta, asadye chilichonse chochokera ku mphesa, ngakhale mbeu zake kapena makungu ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi yonse imene ali Mnaziri, asamadye chilichonse chopangidwa kuchokera ku mphesa ngakhale mbewu zake kapena makungu ake.’ |
Ichi ndi chilamulo cha Mnaziri wakuwinda, ndi cha chopereka chake cha Yehova chifukwa cha kusala kwake, pamodzi nacho chimene dzanja lake likachipeza; azichita monga mwa chowinda chake anachiwinda, mwa chilamulo cha kusala.
azisala vinyo ndi kachasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kachasu wosasa, kapena chakumwa chonse cha mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.
Masiku onse a chowinda chake chakusala, lumo lisapite pamutu pake; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lake zimeretu.
Chilichonse chichokera kumpesa asadyeko, asamwe vinyo kapena choledzeretsa, kapena kudya chilichonse chodetsa; zonse ndinamlamulira azisunge.