Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 6:3 - Buku Lopatulika

3 azisala vinyo ndi kachasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kachasu wosasa, kapena chakumwa chonse cha mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 azisala vinyo ndi kachasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kachasu wosasa, kapena chakumwa chonse cha mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 asamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa. Asamwe vinyo wopangidwa ndi mphesa kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo asamwe madzi amphesa kapena kudya mphesa zaziŵisi kapena zouma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 sayenera kumwa vinyo kapena zakumwa zosasa ndipo asamamwe chakumwa chilichonse cha mphesa. Asamamwe madzi a mphesa kapena kudya mphesa zaziwisi kapena zowuma.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:3
15 Mawu Ofanana  

Usamamwa vinyo, kapena choledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'chihema chokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;


Ndipo ndinaukitsa mwa ana anu aneneri, ndi mwa anyamata anu Anaziri. Si momwemo, inu ana a Israele, ati Yehova?


Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera.


Masiku onse a kusala kwake asadye kanthu kopangika ndi mphesa, kuyambira nthanga zake kufikira khungu lake.


Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.


Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;


Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,


Mupewe maonekedwe onse a choipa.


Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang'ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri.


Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.


Chilichonse chichokera kumpesa asadyeko, asamwe vinyo kapena choledzeretsa, kapena kudya chilichonse chodetsa; zonse ndinamlamulira azisunge.


Chifukwa chake udzisamalire, usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chinthu chilichonse chodetsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa