Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 6:21 - Buku Lopatulika

21 Ichi ndi chilamulo cha Mnaziri wakuwinda, ndi cha chopereka chake cha Yehova chifukwa cha kusala kwake, pamodzi nacho chimene dzanja lake likachipeza; azichita monga mwa chowinda chake anachiwinda, mwa chilamulo cha kusala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ichi ndi chilamulo cha Mnaziri wakuwinda, ndi cha chopereka chake cha Yehova chifukwa cha kusala kwake, pamodzi nacho chimene dzanja lake likachipeza; azichita monga mwa chowinda chake anachiwinda, mwa chilamulo cha kusala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 “Limeneli ndilo lamulo la munthu amene alumbira kuti akhale Mnaziri. Zinthu zake zimene apereka kwa Chauta zikhale zomwe adalumbirira pa unaziri, osaŵerengera zina zimene angathe kupereka moonjezerapo. Zimene adalumbira kuti adzachita, achite momwemo potsata lamulo la kudzipereka kuti adzakhale Mnaziri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 “Ili ndi lamulo la Mnaziri yemwe walonjeza kudzipereka kwa Yehova podzipatula yekha kuphatikiza pa zomwe angathe kukwaniritsa. Ayenera kukwaniritsa lonjezo lomwe wachitalo potsata lamulo la Mnaziri.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:21
7 Mawu Ofanana  

Monga momwe anakhoza anapereka kuchuma cha ntchitoyi madariki agolide zikwi zisanu ndi chimodzi, miyeso ya mina ya siliva zikwi zisanu, ndi malaya a ansembe zana limodzi.


Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonjeza chowinda cha Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova;


ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ichi nchopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.


Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa