Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake.
Numeri 6:13 - Buku Lopatulika Ndipo chilamulo cha Mnaziri, atatha masiku a kusala kwake ndi ichi: azidza naye ku khomo la chihema chokomanako; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chilamulo cha Mnaziri, atatha masiku a kusala kwake ndi ichi: azidza naye ku khomo la chihema chokomanako; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Lamulo la Mnaziri pamene nthaŵi ya kudzipereka kwake yatha, nali: abwere naye pakhomo pa chihema chamsonkhano, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. |
Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake.
Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwake m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa mu Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.
Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye mu Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,