Numeri 6:10 - Buku Lopatulika Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe; ku khomo la chihema chokomanako; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lachisanu ndi chitatu abwere ndi nkhunda ziŵiri kapena njiŵa ziŵiri kwa wansembe pakhomo pa chihema chamsonkhano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono pa tsiku lachisanu ndi chitatu abweretse nkhunda ziwiri kapena mawunda awiri anjiwa kwa wansembe pa khomo lolowera ku tenti ya msonkhano. |
Ndipo chopereka chake cha kwa Yehova chikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera nacho chopereka chake chikhale cha njiwa, kapena cha maunda.
Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwake pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwanawankhosa wa chaka chimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yauchimo, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe;
limodzi la nsembe yauchimo, ndi lina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova iye wakuyeretsedwa.
Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike pamaso pa Yehova pa khomo la chihema chokomanako, nazipereke kwa wansembe;
Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la chihema chokomanako.
amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.