Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 6:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tsono pa tsiku lachisanu ndi chitatu abweretse nkhunda ziwiri kapena mawunda awiri anjiwa kwa wansembe pa khomo lolowera ku tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe; ku khomo la chihema chokomanako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu abwere ndi nkhunda ziŵiri kapena njiŵa ziŵiri kwa wansembe pakhomo pa chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:10
11 Mawu Ofanana  

Atatha kuyeretsedwa adikirebe masiku asanu ndi awiri kuti ayere ndithu.


“ ‘Koma ngati chopereka kwa Yehova ndi nsembe yopsereza ya mbalame, ndiye ikhale njiwa kapena mawunda.


“ ‘Masiku ake wodziyeretsa akatha, kaya ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la tenti ya msonkhano kuti ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi chiwunda cha nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yopepesera machimo.


imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka chachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu woti ayeretsedwe.


Pa tsiku la chisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri kapena mawunda a nkhunda awiri ndi kubwera nazo pamaso pa Yehova pa khomo pa tenti ya msonkhano ndipo azipereke kwa wansembe.


Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mkaziyo atenge njiwa ziwiri kapena mawunda awiri, ndipo abwere nazo kwa wansembe pa khomo la Tenti ya Msonkhano.


Iye anaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha machimo athu ndipo anaukitsidwa ndi kukhala ndi moyo kuti tilungamitsidwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa