Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna, ndipo sadzachitira chifundo tsiku lobwezera chilango.
Numeri 5:14 - Buku Lopatulika ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti achitire nsanje mkazi wake, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amchitire mkazi wake nsanje angakhale sanadetsedwe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti achitire nsanje mkazi wake, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amchitire mkazi wake nsanje angakhale sanadetsedwe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo mwamuna wakeyo akayamba kuchitira nsanje mkazi wake amene wadziipitsayo, kapena akayamba kuchitira nsanje mkazi wakeyo ngakhale sadadziipitse, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mwamuna wake ndi kuyamba kuchita nsanje ndi kukayikira mkazi wakeyo kuti ndi wodetsedwa, komanso ngati amuchitira nsanje ndi kumukayikira ngakhale asanadzidetse, |
Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna, ndipo sadzachitira chifundo tsiku lobwezera chilango.
Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova.
Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.
kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse.