Numeri 4:42 - Buku Lopatulika Ndipo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaŵerenganso ana a Merari potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amerari anawawerenga monga mwa mafuko ndi mabanja awo. |
ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mu udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;
Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Geresoni, onse akutumikira m'chihema chokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova.
kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu kuti agwire ntchito m'chihema chokomanako,