ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mu udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;
Numeri 4:38 - Buku Lopatulika Ndipo ana owerengedwa a Geresoni, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana owerengedwa a Geresoni, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaŵerenganso ana a Geresoni potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ageresoni anawerengedwanso monga mwa mafuko ndi mabanja awo. |
ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mu udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;
Owerengedwa ao, powawerenga amuna onse, kuyambira mwana wa mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.
Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'chihema chokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.
kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito m'chihema chokomanako,