Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 4:37 - Buku Lopatulika

37 Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'chihema chokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'chihema chokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Chimenecho ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'mabanja a Akohati, onse amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Ichi chinali chiwerengero cha mafuko a Akohati onse omwe ankatumikira mu tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:37
7 Mawu Ofanana  

Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa Iye ndi ana a Israele m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.


Ndipo Mose anawawerenga monga mwa mau a Yehova, monga adamuuza.


Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.


ndipo owerengedwa ao monga mwa mabanja ao ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.


Ndipo ana owerengedwa a Geresoni, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao,


kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa kugwira ntchito ya utumikiwu, ndiyo ntchito ya akatundu m'chihema chokomanako;


Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa