Ichi ndi chiwerengo cha zinthu za chihema, chihema cha mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, achite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.
Numeri 4:28 - Buku Lopatulika Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Geresoni m'chihema chokomanako; ndipo Itamara mwana wa Aroni wansembe ayang'anire udikiro wao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Geresoni m'chihema chokomanako; ndipo Itamara mwana wa Aroni wansembe ayang'anire udikiro wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Imeneyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Ageresoni m'chihema chamsonkhano, ndipo woyang'anira ntchitoyo akhale Itamara, mwana wa wansembe Aroni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyi ndiye ntchito ya fuko la Ageresoni ku tenti ya msonkhano. Ntchito zawo zichitike motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni. |
Ichi ndi chiwerengo cha zinthu za chihema, chihema cha mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, achite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.
Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake aamuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.
Kunena za ana a Merari, Uwawerenge monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao.
Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Merari, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako, mowauza Itamara mwana wa Aroni wansembe.