Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zotchingira za kubwalo za nsalu yabafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana;
Numeri 4:26 - Buku Lopatulika ndi nsalu zotchingira za pabwalo, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo lili pa chihema ndi paguwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za ntchito zao, ndi zonse achita nazo; m'menemo muli ntchito zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi nsalu zochingira za pabwalo, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo lili pa Kachisi ndi pa guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za ntchito zao, ndi zonse achita nazo; m'menemo muli ntchito zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Azinyamulanso nsalu zochingira bwalo, nsalu yochingira khomo la pa chipata cha bwalo lozungulira malo opatulika ndi guwa, zingwe zake ndi zipangizo zina zonse zofunika. Agwire ntchito zonse zimene aŵapatse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero makatani wotchingira bwalo lozungulira chihema ndi guwa, katani ya pa khomo, zingwe ndi zida zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito mʼchihema. Ageresoni azichita zonse zofunika kuchitika ndi zinthu zimenezi. |
Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zotchingira za kubwalo za nsalu yabafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana;
Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zotchingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;
Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake aamuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.