ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Numeri 36:6 - Buku Lopatulika Cholamulira Yehova za ana aakazi a Zelofehadi ndi ichi, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ake; komatu akwatibwe nao a banja la fuko la makolo ao okhaokha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Cholamulira Yehova za ana akazi a Zelofehadi ndi ichi, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ake; komatu akwatibwe nao a banja la fuko la makolo ao okhaokha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zomwe Chauta akulamula za ana aakazi a Zelofehadi ndi izi: Aloleni akwatiwe ndi yemwe akumufuna, malinga akwatiwe ndi a m'banja la fuko la makolo ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Izi ndi zimene Yehova akulamula kwa ana aakazi a Zelofehadi: Atha kukwatiwa ndi aliyense amene angakondweretsedwe naye koma zingakhale bwino atakwatiwa mʼfuko la abambo awo |
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Nafa Eleazara wopanda ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndi asuweni ao ana a Kisi anawatenga akhale akazi ao.
Ana aakazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.
Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chao chinakhala m'fuko la banja la atate wao.
Ndipo Mose analamulira ana a Israele monga mwa mau a Yehova, nati, Fuko la ana a Yosefe linena zoona.
Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?