Ndipo m'dziko monse simunapezeke akazi okongola ngati ana aakazi a Yobu, nawapatsa cholowa atate wao pamodzi ndi alongo ao.
Numeri 36:2 - Buku Lopatulika nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake aakazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake akazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwowo adati, “Chauta adakulamulani inu mbuyathu kuti mutachita maere, mupatse Aisraele dziko, kuti likhale choloŵa chao. Ndiponso inu mbuyathu, Chauta adakulamulani kuti mupatse choloŵa cha mbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anati, “Pamene Yehova analamula mbuye wanga kuti apereke dziko ngati cholowa kwa Aisraeli mwa maere, anakulamulani inu kupereka cholowa cha mʼbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi. |
Ndipo m'dziko monse simunapezeke akazi okongola ngati ana aakazi a Yobu, nawapatsa cholowa atate wao pamodzi ndi alongo ao.
Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.
Ndipo akakwatibwa nao ana aamuna a mafuko ena a ana a Israele, achichotse cholowa chao ku cholowa cha makolo athu, nachionjeze ku cholowa cha fuko limene adzakhalako; chotero achichotse ku maere a cholowa chathu.
nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.