Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 32:41 - Buku Lopatulika

Ndipo Yairi mwana wa Manase ananka nalanda midzi yao, naitcha Havoti-Yairi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yairi mwana wa Manase ananka nalanda midzi yao, naitcha Havoti-Yairi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yairi wa fuko la Manase adapita kukalanda midzi ina naitcha Havoti-Yairi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yairi, mwana wa Manase analanda midzi yambiri ya Giliyadi ndi kuyitcha kuti Havoti-Yairi.

Onani mutuwo



Numeri 32:41
5 Mawu Ofanana  

Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;


Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino).


Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basani lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basani, ndi mizinda yonse ya Yairi, yokhala mu Basani, mizinda makumi asanu ndi limodzi;


Ndipo anali nao ana aamuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo mizinda makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi.