koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko aoao pakati pa inu m'dziko la Kanani.
Numeri 32:31 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzachita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzachita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo zidzukulu za Gadi ndi za Rubeni zidayankha kuti, “Ife atumiki anu tidzachita zomwe Chauta watiwuza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Agadi ndi Arubeni anayankha kuti, “Antchito anu adzachita zimene Yehova wanena. |
koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko aoao pakati pa inu m'dziko la Kanani.
Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma cholowa chathuchathu chikhale tsidya lino la Yordani.
Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzachita, ndipo kulikonse mutitumako tidzamuka.