Dzimangireni mizinda ya ana anu, ndi makola a zoweta zanu; ndipo muzichite zotuluka m'kamwa mwanu.
Numeri 32:25 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzachita monga mbuyanga alamulira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzachita monga mbuyanga alamulira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ana a Gadi ndi ana a Rubeni adayankha Mose kuti, “Atumiki anu adzachitadi monga momwe inu mbuyathu mwalamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Agadi ndi Arubeni anati kwa Mose, “Ife antchito anu tidzachita monga mbuye wathu mwalamulira. |
Dzimangireni mizinda ya ana anu, ndi makola a zoweta zanu; ndipo muzichite zotuluka m'kamwa mwanu.
Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'mizinda ya ku Giliyadi;
Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzachita, ndipo kulikonse mutitumako tidzamuka.