Ndipo Mose anasankha amuna anzeru mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi.
Numeri 30:1 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ananena ndi akulu a mafuko a ana a Israele, nati, Chinthu anachilamulira Yehova ndi ichi: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ananena ndi akulu a mafuko a ana a Israele, nati, Chinthu anachilamulira Yehova ndi ichi: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adauza atsogoleri a mafuko a Aisraele kuti, Chauta walamula kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anawuza Aisraeli onse zonse zimene Yehova anamulamula. Iye anati, “Zimene Yehova walamula ndi izi: |
Ndipo Mose anasankha amuna anzeru mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi.
Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikiro zonse zimene adamlamulira.
akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;
Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako.