Numeri 3:50 - Buku Lopatulika analandira ndalamazo kwa oyamba kubadwa a ana a Israele; masekeli chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 analandira ndalamazo kwa oyamba kubadwa a ana a Israele; masekeli chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adatenga ndalama zasiliva kwa ana achisamba a Aisraele okwanira 1,365, molingana ndi kaŵerengedwe ka masekeli asiliva a ku Chihema cha Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anatenga masekeli a siliva okwana 1,365 molingana ndi masekeli a ku malo opatulika, kuchokera kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisraeli. |
Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ake ndalama zoombola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose.
monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi anaang'ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi kumalo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha.
podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu:
Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;