Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu aamuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.
Numeri 3:45 - Buku Lopatulika Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Utenge Alevi m'malo mwa ana onse achisamba pakati pa Aisraele, utengenso ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe za Aisraele. Aleviwo ndi anga, Ine ndine Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso zoweta zonse za Alevi mʼmalo mwa zoweta za Aisraeli. Alevi ndi anga. Ine ndine Yehova. |
Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu aamuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.
Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kuti chipangano changa chikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu.
Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.
Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga.
Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele.