Numeri 3:26 - Buku Lopatulika ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku chihema, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku Kachisi, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa nsalu zochingira bwalo, nsalu zochingira khomo la bwalo lozungulira chihema cha Mulungu ndi guwa lansembe, ndiponso zingwe zake. Ankagwira ntchito zonse zokhudza zimenezi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndi makatani wotchinga bwalo, katani ya pa chipata cholowera ku bwalo lozungulira Chihema ndi guwa lansembe, zingwe ndi zonse zokhudzana ndi ntchito yawo. |
Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.