Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 29:3 - Buku Lopatulika

ndi nsembe yao yaufa, ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombeyo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi nsembe yao yaufa, ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombeyo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Muperekenso chopereka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzipereka chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa yayimuna iliyonse muzipereka makilogalamu awiri.

Onani mutuwo



Numeri 29:3
4 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.


ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;


Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;


ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;