Numeri 28:5 - Buku Lopatulika ndi limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muziperekanso kilogaramu limodzi la ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta aolivi oyenga bwino okwanira lita limodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muziperekanso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi. |
Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m'mawa ndi m'mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusakaniza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha.
Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani.
Ndiyo nsembe yopsereza kosalekeza, yoikika kuphiri la Sinai, ichite fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;