Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;
Numeri 27:23 - Buku Lopatulika namuikira manja ake, namlangiza monga Yehova adanena ndi dzanja la Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 namuikira manja ake, namlangiza monga Yehova adanena ndi dzanja la Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adamsanjika manja, nampatsa udindo monga momwe Chauta adamlangizira kudzera mwa Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anamusanjika manja ndi kumupatsa mphamvu, monga Yehova ananenera kudzera mwa Mose. |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;
numuimike pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; numlangize pamaso pao.
Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza; natenga Yoswa namuimitsa pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse;
Ndipo ndinauza Yoswa muja, ndi kuti, Maso ako anapenya zonse Yehova Mulungu wanu anawachitira mafumu awa awiri; momwemo Yehova adzachitira maufumu onse kumene muolokerako.
Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao.
Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israele m'dziko limene ndinawalumbirira; ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.
Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ake; ndi ana a Israele anamvera iye, nachita monga Yehova adauza Mose.