mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
Numeri 27:2 - Buku Lopatulika Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga; ndi khamu lonse, pakhomo pa chihema chokomanako, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga; ndi khamu lonse, pakhomo pa chihema chokomanako, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwoŵa adakaima pamaso pa Mose, pa wansembe Eleazara, pa atsogoleri, ndiponso pamaso pa mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, nati, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pa chipata cha tenti ya msonkhano pamaso pa Mose, wansembe Eliezara, atsogoleri ndi anthu onse, ndipo anati, |
mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
Pamenepo anayandikiza ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.
Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.
Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.
Ndipo akulu a makolo a mabanja a ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akulu a makolo a ana a Israele;
Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;