Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?
Numeri 27:14 - Buku Lopatulika popeza munapikisana nao mau anga m'chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pamadziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba mu Kadesi, m'chipululu cha Zini. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 popeza munapikisana nao mau anga m'chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pa madziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba m'Kadesi, m'chipululu cha Zini. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa chifukwa simudamvere mau anga m'chipululu cha Zini pa nthaŵi imene mpingo udandiwukira ku madzi a Meriba, pamene simudaonetse kuyera kwanga pamaso pao.” (Ameneŵa ndiwo madzi a kasupe wa ku Meriba ku Kadesi, m'chipululu cha Zini.) Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero chifukwa pamene anthu anawukira ku madzi a Meriba mʼchipululu cha Zini, inu nonse simunamvere lamulo londilemekeza Ine ngati Woyera pamaso pawo.” (Awa anali madzi a ku Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini). |
Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?
Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.
Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.
Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.
Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa mu Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.
Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.
pakuti ndidzafa m'dziko muno, osaoloka Yordani; koma inu mudzaoloka, ndi kulandira dziko ili lokoma likhale lanulanu.