Ndi ana aamuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.
Numeri 26:41 - Buku Lopatulika Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneŵa, anthu okwanira 45,600, ndiwo anali a m'mabanja a Benjamini, amene adaŵerengedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600. |
Ndi ana aamuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.
Ndipo ana aamuna a Bela ndiwo Aridi ndi Naamani; Aridi, ndiye kholo la banja la Aaridi; Naamani, ndiye kholo la banja la Anaamani.
Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ake ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao.
Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m'mizinda tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala mu Gibea, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri.