ndi Asiriele, ndiye kholo la banja la Aasiriele; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu;
Numeri 26:30 - Buku Lopatulika Ana a Giliyadi ndiwo: Iyezere, ndiye kholo la banja la Aiyezere; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana a Giliyadi ndiwo: Iyezere, ndiye kholo la banja la Aiyezere; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana aamuna a Giliyadi anali aŵa: Iyezere anali kholo la banja la Aiyezere. Heleki anali kholo la banja la Aheleki. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi; kuchokera mwa Iyezeri, fuko la Aiyezeri; kuchokera mwa Heleki, fuko la Aheleki; |
ndi Asiriele, ndiye kholo la banja la Aasiriele; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu;
Ndipo maere anagwera ana ena otsala a Manase monga mwa mabanja ao; ana a Abiyezere ndi ana a Heleki, ndi ana a Asiriele, ndi ana a Sekemu ndi ana a Hefere, ndi ana a Semida; awa ndi ana aamuna a Manase mwana wa Yosefe, monga mwa mabanja ao.
Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala mu Ofura, wa Yowasi Mwabiyezere; ndi mwana wake Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidiyani.
Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalitcha Yehova-ndiye-mtendere; likali mu Ofura wa Aabiyezere ndi pano pomwe.
Koma mzimu wa Yehova unavala Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abiyezere analalikidwa kumtsata iye.
Koma ananena nao, Ndachitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efuremu sikuposa kutchera mphesa kwa Abiyezere?