Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 8:2 - Buku Lopatulika

2 Koma ananena nao, Ndachitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efuremu sikuposa kutchera mphesa kwa Abiyezere?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Koma ananena nao, Ndachitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efuremu sikuposa kutchera mphesa kwa Abiyezere?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iye adaŵayankha kuti, “Ndachita chiyani ine kuyerekeza ndi zimene mwachita inu? Kodi zimene mwachita inu Aefuremu si zazikulu koposa zimene fuko langa la Abiyezere lachita?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Koma iye anawayankha kuti, “Nʼchiyani ndachita kuyerekeza ndi zimene mwachita inu? Kodi zimene mwachita inu Aefereimu si zazikulu kuposa zimene fuko langa la Abiezeri lachita?

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 8:2
11 Mawu Ofanana  

Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.


Ana a Giliyadi ndiwo: Iyezere, ndiye kholo la banja la Aiyezere; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki;


Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala mu Ofura, wa Yowasi Mwabiyezere; ndi mwana wake Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidiyani.


Koma mzimu wa Yehova unavala Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abiyezere analalikidwa kumtsata iye.


Ndipo amuna a Efuremu anati kwa iye, Ichi watichitira nchiyani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidiyani? Natsutsana naye kolimba.


Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midiyani, Orebu ndi Zeebu, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa