Numeri 26:26 - Buku Lopatulika Ana aamuna a Zebuloni monga mwa mabanja ao ndiwo: Seredi, ndiye kholo la banja la Aseredi; Eloni, ndiye kholo la banja la Aeloni; Yaleele, ndiye kholo la banja la Ayaleele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana amuna a Zebuloni monga mwa mabanja ao ndiwo: Seredi, ndiye kholo la banja la Aseredi; Eloni, ndiye kholo la banja la Aeloni; Yaleele, ndiye kholo la banja la Ayaleele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Potsata mabanja ao ana aamuna a Zebuloni anali aŵa: Seredi anali kholo la banja la Aseredi. Eloni anali kholo la banja la Aeloni. Yaleele anali kholo la banja la Ayaleele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Seredi, fuko la Aseredi; kuchokera mwa Eloni, fuko la Aeloni; kuchokera mwa Yahaleeli, fuko la Ayahaleeli. |
A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;