Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu.
Numeri 24:25 - Buku Lopatulika Ndipo Balamu anauka, namuka nabwerera kumalo kwake; ndi Balaki yemwe ananka njira yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Balamu anauka, namuka nabwerera kumalo kwake; ndi Balaki yemwe ananka njira yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Balamu adanyamuka nabwerera kwao. Balaki nayenso adapita kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Balaamu ananyamuka ndi kubwerera kwawo ndipo Balaki anapitanso njira yake. |
Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu.
Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzachitira anthu anu, masiku otsiriza.
Ndipo Israele anakhala mu Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana aakazi a Mowabu;
Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.
Ana a Israele anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo.