Numeri 24:21 - Buku Lopatulika Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lake, nati, kwanu nkokhazikika, wamanga chisa chako m'thanthwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lake, nati, kwanu nkokhazikika, wamanga chisa chako m'thanthwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adayang'ana Akeni, tsono adayamba kulankhula nati, “Ngakhale malo amene mukukhalawo ngopanda zovuta, monga chisa chomangidwa pa thanthwe, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anaonanso Akeni ndipo ananena uthenga wake, “Malo amene mukukhalamo ndi otetezedwa, chisa chanu chinayikidwa pa thanthwe; |
Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m'chisa changa; ndipo ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga.
Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mzinda wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.
Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke.