popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.
Numeri 24:11 - Buku Lopatulika Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake, chokani, kazipitani kwanu. Ndidaakuuzani kuti ndidzakupatsani mphotho, koma Chauta wakana kuti muilandire mphothoyo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.” |
popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.
Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumize kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? Sindikhoza kodi kukuchitira ulemu?
Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti,
Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.
Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,
Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.