pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni.
Numeri 23:17 - Buku Lopatulika Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adabwerera kwa Balaki, ndipo adangoona akuimirira pafupi ndi nsembe yake yopsereza, ali ndi akalonga a ku Mowabu aja. Balaki adamufunsa kuti, “Nanga Chauta wakuuzani zotani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anapita kwa iye ndipo anamupeza atayimirira pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu a ku Mowabu. Balaki anafunsa Balaamu kuti, “Yehova wayankhula chiyani?” |
pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni.
Ndipo Yehova anakomana naye Balamu, naika mau m'kamwa mwake, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti.
Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?
Ndipo anati, Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine. Mulungu akulange, ndi kuonjezapo, ngati undibisira chimodzi cha zonse zija adanena nawe.