popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.
Numeri 23:11 - Buku Lopatulika Pamenepo Balaki anati kwa Balamu, Wandichitiranji? Ndinakutenga utemberere adani anga, ndipo taona, wawadalitsa ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Balaki anati kwa Balamu, Wandichitiranji? Ndinakutenga utemberere adani anga, ndipo taona, wawadalitsa ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Balaki adafunsa Balamu kuti, “Mwandichitira zotani? Suja ndidakuitanani kuti mudzatemberere adani anga, koma m'malo mwake mwangoŵadalitsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Balaki anati kwa Balaamu, “Wandichitira chiyani? Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, ndipo taona, sunachite chilichonse koma kuwadalitsa!” |
popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.
Taonani, anthu awa adatuluka mu Ejipito aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapirikitsa.
popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.
Ndipo anayankha nati, Chimene achiika m'kamwa mwanga Yehova, sindiyenera kodi kunena ichi?
Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.