Numeri 21:32 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda midzi yake, napirikitsa Aamori a komweko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda milaga yake, napirikitsa Aamori a komweko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adatuma anthu kuti akazonde Yazere. Ndipo Aisraele adagwira midzi yake, napirikitsa Aamori amene anali kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose atatumiza azondi ku Yazeri, Aisraeliwo analanda midzi yozungulira ndi kuthamangitsa Aamori omwe ankakhala kumeneko. |
Naoloka Yordani, namanga zithando ku Aroere ku dzanja lamanja kwa mzinda uli pakati pa chigwa cha Gadi, ndi ku Yazere;
Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mphakasa ndi mphesa zako.
Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.
Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,
Ndipo malire ao ndiwo Yazere, ndi mizinda yonse ya Giliyadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroere, wokhala chakuno cha Raba;
Ndipo ndinatuma mavu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai.