Yeremiya 48:32 - Buku Lopatulika32 Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mphakasa ndi mphesa zako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201432 Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa32 Ndikulira anthu a ku Sibima kupambana m'mene ndidalirira anthu a ku Yazere. Iwe mzinda wa Sibima, uli ngati mpesa umene nthambi zake zidatambalala mpaka ku nyanja, kukafika mpaka ku Yazere. Woononga wasakaza zipatso zako zam'chilimwe, wasakaza mipesa yako yonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero32 Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri. Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesa imene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja; zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri. Wowononga wasakaza zipatso zake zachilimwe ndi mpesa. Onani mutuwo |