Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi;
Numeri 21:27 - Buku Lopatulika Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti, Idzani ku Hesiboni, mzinda wa Sihoni umangike, nukhazikike. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti, Idzani ku Hesiboni, mudzi wa Sihoni umangike, nukhazikike. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake oimba ndakatulo amati, “Bwerani ku Hesiboni, mzindawu umangidwenso, tiyeni timange mzinda wa Sihoni kuti ukhazikikenso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake alakatuli amati: “Bwerani ku Hesiboni, mzindawo umangidwenso; mzinda wa Sihoni ukhazikike. |
Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi;
pamenepo udzaimbira mfumu ya ku Babiloni nyimbo iyi yanchinchi, ndi kuti, Wovuta wathadi? Mudzi wagolide wathadi!
Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wochulukitsa zimene sizili zake? Mpaka liti? Iye wodzisenzera zigwiriro.
Chifukwa chake, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova, Waheba mu Sufa, ndi miyendo ya Arinoni;
Popeza Hesiboni ndiwo mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Mowabu, nilanda dziko lake m'dzanja lake kufikira Arinoni.
Popeza moto unatuluka mu Hesiboni, chirangali cha moto m'mzinda wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni.