Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe.
Numeri 21:15 - Buku Lopatulika ndi zigwa za miyendoyo zakutsikira kwao kwa Ari, ndi kuyandikizana ndi malire a Mowabu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi zigwa za miyendoyo zakutsikira kwao kwa Ari, ndi kuyandikizana ndi malire a Mowabu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ku matsitso a zigwa amene afika mpaka ku Ari, nakhudza malire a dziko la Mowabu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ku matsitso a zigwa amene afika mpaka ku Ari nakhudza malire a dziko la Mowabu.” |
Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe.
Chifukwa chake, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova, Waheba mu Sufa, ndi miyendo ya Arinoni;
Popeza moto unatuluka mu Hesiboni, chirangali cha moto m'mzinda wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni.
monga anandichitira ana a Esau akukhala mu Seiri, ndi Amowabu akukhala mu Ari; kufikira nditaoloka Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.