Ndipo ana a Israele ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wake; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira.
Numeri 20:18 - Buku Lopatulika Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingatuluke kukomana nawe ndi lupanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingatuluke kukomana nawe ndi lupanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Edomu adayankha kuti, “Musadzere kuno, kuti ndingafike kudzakubayani ndi lupanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Edomu anayankha kuti, “Musadutse kuno: Mukangoyesera tidzabwera ndi kumenyana nanu ndi lupanga.” |
Ndipo ana a Israele ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wake; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira.
Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anatulukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.
Ndipo Sihoni sanalole Israele apitire m'malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, nadzakomana naye Israele m'chipululu, nafika ku Yahazi, nathira nkhondo pa Israele.
Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.
Ndi Edomu adzakhala akeake, Seiri lomwe lidzakhala lakelake, ndiwo adani ake; koma Israele adzachita zamphamvu.
monga anandichitira ana a Esau akukhala mu Seiri, ndi Amowabu akukhala mu Ari; kufikira nditaoloka Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa.