Numeri 2:5 - Buku Lopatulika Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Isakara; ndipo kalonga wa ana a Isakara ndiye Netanele mwana wa Zuwara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Isakara; ndipo kalonga wa ana a Isakara ndiye Netanele mwana wa Zuwara. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Isakara. Mtsogoleri wa fuko la Isakaralo ndi Netanele mwana wa Zuwara, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Fuko la Isakara lidzamanga pafupi ndi Yuda. Mtsogoleri wa gulu la Isakara ndi Netanieli mwana wa Zuwara. |
Ndipo khamu lake, ndi owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri, mphambu zinai, kudza mazana asanu ndi limodzi.
Ndipo khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Netanele mwana wa Zuwara.