Numeri 2:19 - Buku Lopatulika Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo ankhondo ake ngokwanira 40,500. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 40,500. |
Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.
Ndipo oyandikizana naye ndiwo a fuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliele mwana wa Pedazuri.
Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana aamuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.