Numeri 2:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: |
Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao.
Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira.
akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;