Numeri 16:47 - Buku Lopatulika Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo chofukiza nawachitira anthu chowatetezera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo chofukiza nawachitira anthu chowatetezera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Aroni adatenga chofukizira, nathamangira pakati penipeni pa msonkhano. Ndipo adangoona mliri utayamba kale pa anthuwo. Tsono adathira lubani, nachita mwambo wopepesera machimo a anthuwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Aaroni anachita monga ananenera Mose, nathamangira mʼkatikati mwa gulu la anthuwo. Pamenepo nʼkuti mliri utayamba kale pakati pa anthu aja ndipo Aaroni anafukiza lubani ndi kupereka nsembe yopepesera machimo awo. |
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mbale yako yofukiza, nuikemo moto wa ku guwa la nsembe, nuikepo chofukiza, nufulumire kumuka ku khamulo, nuwachitire chowatetezera; pakuti watuluka mkwiyo pamaso pa Yehova; wayamba mliri.
ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zake zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anachita nsanje chifukwa cha Mulungu wake, anawachitira ana a Israele chowatetezera.